Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 22:13 - Buku Lopatulika

13 Andiyasamira m'kamwa mwao, ngati mkango wozomola ndi wobangula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Andiyasamira m'kamwa mwao, ngati mkango wozomola ndi wobangula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Andiyasamira kukamwa, ngati mkango wobangula wofuna kundikadzula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Mikango yobangula pokadzula nyama, yatsekula kwambiri pakamwa pawo kulimbana nane.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 22:13
13 Mawu Ofanana  

Iwo anandiyasamira pakamwa pao; anandiomba pama ndi kunditonza; asonkhana pamodzi kunditsutsa.


Afanana ndi mkango wofuna kumwetula, ndi msona wa mkango wakukhala mobisalamo.


ndipulumutseni m'kamwa mwa mkango; inde mwandiyankha ine ndili pa nyanga za njati.


Onse akundipenya andiseka; akwenzula, apukusa mutu, nati,


Ambuye, mudzapenyererabe nthawi yanji? Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao, wanga wa wokha kwa misona ya mkango.


Ndipo andiyasamira m'kamwa mwao; nati, Hede, Hede, diso lathu lidachipenya.


kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango, ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.


Adani ako onse ayasamira pa iwe, atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza; ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.


Adani athu onse anatiyasamira.


Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa