Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 22:14 - Buku Lopatulika

14 Ndathiridwa pansi monga madzi, ndipo mafupa anga onse anaguluka. Mtima wanga ukunga sera; wasungunuka m'kati mwa matumbo anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndathiridwa pansi monga madzi, ndipo mafupa anga onse anaguluka. Mtima wanga ukunga sera; wasungunuka m'kati mwa matumbo anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Moyo wanga watayika ngati madzi, mafupa anga aweyeseka. Mtima wanga uli ngati sera, wasungunuka m'kati mwanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Ine ndatayika pansi ngati madzi ndipo mafupa anga onse achoka mʼmalo mwake. Mtima wanga wasanduka phula; wasungunuka mʼkati mwanga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 22:14
15 Mawu Ofanana  

Iwo anandiyasamira pakamwa pao; anandiomba pama ndi kunditonza; asonkhana pamodzi kunditsutsa.


Pakuti Mulungu walefula mtima wanga, ndi Wamphamvuyonse wandiopsa.


Ndipo tsopano moyo wanga udzitsanulira m'kati mwanga; masiku akuzunza andigwira.


Ndikhoza kuwerenga mafupa anga onse; iwo ayang'ana nandipenyetsetsa ine.


Pakuti moyo wanga watha ndi chisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo. Mphamvu yanga yafooka chifukwa cha kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.


Ndipo andiyasamira m'kamwa mwao; nati, Hede, Hede, diso lathu lidachipenya.


Muwachotse monga utsi uchotseka; monga phula lisungunuka pamoto, aonongeke oipa pamaso pa Mulungu.


Adani athu onse anatiyasamira.


Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m'chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana.


Ndiye mopanda kanthu mwakemo ndi mwachabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m'zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka.


Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa; khalani pano muchezere pamodzi ndi Ine.


Ndipo pokhala Iye m'chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.


Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.


Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapirikitsa kuyambira pachipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa