Masalimo 66:3 - Buku Lopatulika Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muuzeni Mulungu kuti, “Ntchito zanu nzodabwitsa kwambiri. Mphamvu zanu nzazikulu, kotero kuti adani anu amakuŵeramirani moopa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu! Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu. |
Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa; ndiye mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.
Mudzatiyankha nazo zoopsa m'chilungamo, Mulungu wa chipulumutso chathu; ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi, ndi cha iwo okhala kutali kunyanja.
Dzudzulani chilombo cha m'bango, khamu la mphongo ndi ng'ombe za anthu, yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva; anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.
Ndipo Miriyamu anawayankha, Imbirani Yehova, pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.
Anthu adzalowa m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'maenje apansi, kuthawa kuopsa kwa Yehova, ndi ulemerero wachifumu wake, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu.
Chifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani Inu, mzinda wa mitundu yakuopsa udzakuopani Inu.
Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lao ndi kuziwerenga; azitcha zonse maina ao, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.
Pamene Inu munachita zinthu zoopsa, zimene ife sitinayang'anira, Inu munatsika, mapiri anagwedezeka pamaso panu.
Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.