Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 18:45 - Buku Lopatulika

45 Alendo adzafota, nadzatuluka monjenjemera m'ngaka mwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

45 Alendo adzafota, nadzatuluka monjenjemera m'ngaka mwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

45 Anthu a mitundu ina adataya mtima, adatuluka m'malinga mwao ali njenjenje.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

45 Iwo onse anataya mtima; anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:45
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anakantha Amowabu nawayesa ndi chingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi chingwe chimodzi chathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nayo mitulo.


Pamenepo Davide anaika maboma mu Aramu wa Damasiko. Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kulikonse anamukako.


Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.


Akadawadyetsa naye tirigu wokometsetsa, ndikadakukhutitsanso ndi uchi wa m'thanthwe.


Dziko lirira nilifota, dziko lilefuka nilifota, anthu omveka a padziko alefuka.


Adzanyambita fumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera potuluka m'ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa chifukwa cha iwe.


Wodala iwe, Israele; akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, ndiye chikopa cha thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; ndipo udzaponda pa misanje yao.


Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m'mayendedwe ake.


nanena kwa mapiri ndi matanthwe, Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife kunkhope ya Iye amene akhala pa mpando wachifumu, ndi kumkwiyo wa Mwanawankhosa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa