Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 66:4 - Buku Lopatulika

4 Dziko lonse lapansi lidzakugwadirani, ndipo lidzakuimbirani; ndzaimbira dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Dziko lonse lapansi lidzakugwadirani, ndipo lidzakuimbirani; ndzaimbira dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Anthu onse a pa dziko lapansi amakupembedzani, amaimba nyimbo zotamanda Inu, amaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Dziko lonse lapansi limaweramira inu; limayimba matamando kwa Inu; limayimba matamando pa dzina lanu.” Sela.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 66:4
12 Mawu Ofanana  

Lemekezani Yehova, amitundu onse; muimbireni, anthu onse.


Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.


Mudzatiyankha nazo zoopsa m'chilungamo, Mulungu wa chipulumutso chathu; ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi, ndi cha iwo okhala kutali kunyanja.


Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m'phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzaza ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.


Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.


Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.


Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa