Masalimo 53:1 - Buku Lopatulika Chitsiru chimati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa; kulibe wakuchita bwino. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chitsiru chimati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa; kulibe wakuchita bwino. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mumtima mwake munthu wopusa amati, “Kulibe Mulungu.” Anthu otereŵa ndi oipa, amachita zonyansa, palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chitsiru chimati mu mtima mwake, “Kulibe Mulungu.” Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa; palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino. |
panalinso anyamata ochitirana dama m'dzikomo; iwo amachita monga mwa zonyansitsa za amitundu, amene Yehova anapirikitsa pamaso pa ana a Israele.
Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.
Koma sunayende m'njira zao, kapena kuchita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kuvunda kwako, m'njira zako zonse.
Ngakhale Samariya sanachite theka la zochimwa zako, koma unachulukitsa zonyansa zako, kuwaposa iwowa, ndi kuika abale ako olungama ndi zonyansa zako zonse unazichita.
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.
Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?
chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitire ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamike; koma anakhala opanda pake m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira.
Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;
Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao aamuna ndi ana ao aakazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.
Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda inu m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;