ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake;
Masalimo 47:2 - Buku Lopatulika Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa; ndiye mfumu yaikulu padziko lonse lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa; ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja Chauta Wopambanazonse, ndi woopsa, ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba; Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi! |
ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake;
Mudzatiyankha nazo zoopsa m'chilungamo, Mulungu wa chipulumutso chathu; ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi, ndi cha iwo okhala kutali kunyanja.
Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu; Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake mphamvu ndi chilimbiko. Alemekezeke Mulungu.
Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.
Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.
Mukapanda kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi olembedwa m'buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo Yehova Mulungu wanu;
Musamaopa pamaso pao; popeza Yehova Mulungu wanu ali pakati pa inu, Mulungu wamkulu ndi woopsa.