Malaki 1:14 - Buku Lopatulika14 Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Atembereredwe munthu wonyenga amene amayesa kuchita zimene adalumbirira popereka nsembe yoipa kwa Chauta, pamene ali nayo nkhosa yamphongo yabwino m'khola.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ine ndine Mfumu yaikulu, ndipo dzina langa nlochititsa mantha pakati pa anthu a mitundu yonse.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 “Atembereredwe munthu wachinyengo amene ali ndi nyama yayimuna yabwino mʼgulu la ziweto zake ndipo analumbira kuyipereka, koma mʼmalo mwake nʼkupereka nsembe kwa Ambuye nyama yosayenera. Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Pakuti ndine mfumu yayikulu, dzina langa liyenera kuopedwa pakati pa anthu a mitundu yonse.’ ” Onani mutuwo |