Masalimo 140:5 - Buku Lopatulika Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika, atchera ukonde wa zingwe, anditchera misampha m'mbali mwa njira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika; iwo atchera zingwe za maukonde awo ndipo anditchera misampha pa njira yanga. Sela |
Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.
Pakuti ananditchera ukonde wao m'mbunamo kopanda chifukwa, anakumbira moyo wanga dzenje kopanda chifukwa.
Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.
Ananditchera ukonde apo ndiyenda; moyo wanga wawerama. Anandikumbira mbuna patsogolo panga; anagwa m'kati mwake iwo okha.
Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse.
Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu.
Mfuu umvekedwe m'nyumba zao, pamene muwatengera khamu la nkhondo dzidzidzi; pakuti akumba dzenje lakundigwira ine, anabisira mapazi anga misampha.