Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 18:22 - Buku Lopatulika

22 Mfuu umvekedwe m'nyumba zao, pamene muwatengera khamu la nkhondo dzidzidzi; pakuti akumba dzenje lakundigwira ine, anabisira mapazi anga misampha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Mfuu umvekedwe m'nyumba zao, pamene muwatengera khamu la nkhondo dzidzidzi; pakuti akumba dzenje lakundigwira ine, anabisira mapazi anga misampha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Muŵatumire gulu lankhondo lidzaŵakanthe modzidzimutsa, ndipo kulira kwamantha kumveke m'nyumba zao. Iwotu andikumbira dzenje loti andiponyemo, ndipo atchera mapazi anga msampha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Kulira kumveke kuchokera mʼnyumba zawo mutawatumizira gulu lankhondo mwadzidzidzi kuti liwakanthe. Iwo andikumbira dzenje kuti ndigweremo ndipo atchera msampha mapazi anga.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 18:22
23 Mawu Ofanana  

Odzikuza anandikumbira mbuna, ndiwo osasamalira chilamulo chanu.


Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.


Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga; munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.


Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa; pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.


Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse.


Fuula ndi mau ako iwe mwana wamkazi wa Galimu! Tamva, iwe Laisa! Iwe Anatoti wosauka!


Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu.


Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.


Munthuyo akhale ngati mizinda imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mfuu mamawa, ndi mkuwo pausana;


Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.


Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akutcha misampha; atcha khwekhwe, agwira anthu.


Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udziveke ndi chiguduli, ndi kumvimvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.


tsiku la lipenga ndi lakufuulira mizinda yamalinga, ndi nsanja zazitali za kungodya.


Pomwepo Afarisi anamuka, nakhala upo wakumkola Iye m'kulankhula kwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa