Ndipo tsopano, kamphindi, Yehova Mulungu wathu wationetsa chisomo, kutisiyira chipulumutso, ndi kutipatsa chichiri m'malo mwake mopatulika; kuti Mulungu wathu atipenyetse m'maso mwathu, ndi kutitsitsimutsa pang'ono mu ukapolo wathu.
Masalimo 13:4 - Buku Lopatulika kuti anganene mdani wanga, Ndamgonjetsa; ndipo angakondwere otsutsana nane posunthika ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti anganene mdani wanga, Ndamlaka; ndipo angakondwere otsutsana nane posunthika ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mdani wanga asati, “Ndampambana,” adani anga onse asakondwere poona kuti ndagwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,” ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa. |
Ndipo tsopano, kamphindi, Yehova Mulungu wathu wationetsa chisomo, kutisiyira chipulumutso, ndi kutipatsa chichiri m'malo mwake mopatulika; kuti Mulungu wathu atipenyetse m'maso mwathu, ndi kutitsitsimutsa pang'ono mu ukapolo wathu.
Adani anga asandikondwerere ine monyenga; okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.
Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, msanje wanga, sindidzagwedezeka.
Ndipo adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.
Chifukwa cha zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi: Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira; ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.
Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu padziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu?