Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 1:16 - Buku Lopatulika

16 Chifukwa cha zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi: Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira; ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Chifukwa cha zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi: Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira; ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Chifukwa cha zimenezi ndikulira, misozi ili mbwembwembwe m'masomu. Pakuti wondisangalatsa sali pafupi, wondilimbitsa mtima ali kutali. Anthu anga asiyidwa chifukwa mdani watigonjetsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 “Chifukwa cha zimenezi ndikulira ndipo maso anga adzaza ndi misozi. Palibe aliyense pafupi woti anditonthoze, palibe aliyense wondilimbitsa mtima. Ana anga ali okhaokha chifukwa mdani watigonjetsa.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 1:16
23 Mawu Ofanana  

Adani ao anawasautsanso, nawagonjetsa agwire mwendo wao.


Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu.


Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.


Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.


Iwe wosautsidwa, wobelukabeluka ndi namondwe, wosatonthola mtima, taona, ndidzakhazika miyala yako m'mawangamawanga abwino, ndi kukhazika maziko ako ndi masafiro.


Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.


Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukulu, ndi bala lopweteka kwambiri.


Pakuti ndani adzakuchitira iwe chisoni, Yerusalemu? Ndani adzakulirira iwe? Ndani adzapatukira kudzafunsa za mkhalidwe wako?


Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa chisoni chake? Mtima wanga walefuka m'kati mwa ine.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.


Pakuti imfa yakwera m'mazenera athu, yalowa m'nyumba mwathu; kuchotsa ana kubwalo, ndi anyamata kumiseu.


Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake; mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza: Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu, asanduka adani ake.


Udyo wake unali m'nsalu zake; sunakumbukire chitsiriziro chake; chifukwa chake watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza; taonani, Yehova, msauko wanga, pakuti mdaniyo wadzikuza yekha.


Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mzindawu.


Mtima wao unafuula kwa Ambuye, linga iwe la mwana wamkazi wa Ziyoni, igwe misozi ngati mtsinje usana ndi usiku; usapume kanthawi, asaleke mwana wa diso lako.


Angakhale alera ana ao, koma ndidzawasowetsa, wosatsala munthu; ndithunso tsoka iwowa, pamene ndiwachokera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa