Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mzinda wa Mulungu. Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba.
Masalimo 101:8 - Buku Lopatulika Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko; kuduliratu onse akuchita zopanda pake kumzinda wa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko; kuduliratu onse akuchita zopanda pake kumudzi wa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku ndi tsiku ndidzaononga oipa onse am'dziko. Onse ochita zoipa ndidzaŵachotsa mu mzinda wa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu onse oyipa mʼdziko; ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa mu mzinda wa Yehova. |
Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mzinda wa Mulungu. Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba.
Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokoma kumbali zake za kumpoto, ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi, mzinda wa mfumu yaikulu.
Monga tidamva, momwemo tidapenya m'mzinda wa Yehova wa makamu, m'mzinda wa Mulungu wathu, Mulungu adzaukhazikitsa kunthawi yamuyaya.
Nyumba ya Davide iwe, Yehova atero, Chita chiweruzo m'mawa, ndi kumlanditsa amene afunkhidwa m'dzanja la wosautsa, kungatuluke kupsa mtima kwanga ngati moto, ndi kutentha kosazimika, chifukwa cha ntchito zanu zoipa.
Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efuremu adzabwerera kunka ku Ejipito; ndipo adzadya chakudya chodetsa mu Asiriya.
Tamvanitu ichi, akulu a nyumba ya Yakobo inu, ndi oweruza a nyumba ya Israele inu, akuipidwa nacho chiweruzo, ndi kupotoza zoongoka zonse.
ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.