Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 46:4 - Buku Lopatulika

4 Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mzinda wa Mulungu. Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mudzi wa Mulungu. Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Koma kuli mtsinje umene mifuleni yake imasangalatsa anthu amumzinda wa Mulungu, malo oyera okhalako Wopambanazonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu, malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 46:4
24 Mawu Ofanana  

Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.


Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha.


Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere; zindifikitse kuphiri lanu loyera, kumene mukhala Inuko.


Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.


Monga tidamva, momwemo tidapenya m'mzinda wa Yehova wa makamu, m'mzinda wa Mulungu wathu, Mulungu adzaukhazikitsa kunthawi yamuyaya.


Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira, mulilemeretsa kwambiri; mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi, muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka.


Mzinda wa Mulungu, inu, akunenerani zakukulemekezani.


Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.


Nkokoma kuyamika Yehova, ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.


Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba kunthawi yonse.


Mitsinje ikweza, Yehova, mitsinje ikweza mkokomo wao; mitsinje ikweza mafunde ao.


Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.


Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja;


Ndipo ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mzinda wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele.


Ndidzafika kwa Yehova ndi chinai, ndi kuwerama kwa Mulungu Wam'mwamba? Kodi ndifike kwa Iye ndi nsembe zopsereza, ndi anaang'ombe a chaka chimodzi?


Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,


Ndipo ananditenga mu Mzimu kunka kuphiri lalikulu ndi lalitali, nandionetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu, wotsika mu Mwamba kuchokera kwa Mulungu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa