Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 9:3 - Buku Lopatulika

3 Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efuremu adzabwerera kunka ku Ejipito; ndipo adzadya chakudya chodetsa mu Asiriya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efuremu adzabwerera kunka ku Ejipito; ndipo adzadya chakudya chodetsa m'Asiriya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Simudzakhalanso m'dziko la Chauta. Aefuremu inu, mudzabwerera ku ukapolo ku Ejipito, mudzadya chakudya choletsedwa ku dziko la Asiriya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Sadzakhalanso mʼdziko la Yehova. Efereimu adzabwerera ku Igupto ndipo mudzadya chakudya chodetsedwa ku Asiriya.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 9:3
24 Mawu Ofanana  

pamenepo Ine ndidzalikha Aisraele kuwachotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba ino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israele adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.


Chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Asiriya analanda Samariya, natenga Aisraele andende, kunka nao ku Asiriya; nawakhalitsa mu Hala, ndi mu Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'mizinda ya Amedi.


Poyamba ndibwezera mphulupulu yao ndi tchimo lao chowirikiza; chifukwa anaipitsa dziko langa ndi mitembo ya zodetsedwa zao, nadzaza cholowa changa ndi zonyansa zao.


Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zake, ndi zabwino zake; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa cholowa changa chonyansa.


Tinagwira mwendo Ejipito ndi Asiriya kuti tikhute zakudya.


Ndipo Yehova anati, Motero ana a Israele adzadya chakudya chao chodetsedwa, mwa amitundu kumene ndidzawaingitsirako.


Koma Daniele anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya cha mfumu, kapena ndi vinyo amamwa; chifukwa chake anapempha mkulu wa adindo amlole asadzidetse.


Adzafika ndi kunjenjemera ngati mbalame ya ku Ejipito, ndi ngati nkhunda m'dziko la Asiriya; ndipo ndidzawakhalitsa m'nyumba zao, ati Yehova


Iye sadzabwerera kunka kudziko la Ejipito, koma Asiriya adzakhala mfumu yake, popeza anakana kubwera.


Ndipo Efuremu ali ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru; aitanira kwa Ejipito, amuka kwa Asiriya.


Abwerera, koma si kwa Wam'mwambayo; akunga uta wosakhulupirika; akalonga ao adzagwa ndi lupanga mwa chipongwe cha lilime lao; ichi ndicho adzawasekera m'dziko la Ejipito.


Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukira mphulupulu yao, nadzalanga zochimwa zao; adzabwerera kunka ku Ejipito.


Pakuti taonani, anachokera chionongeko, koma Ejipito adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m'manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m'mahema mwao.


lingakusanzeni inunso dzikoli, polidetsa inu, monga linasanza mtundu wa anthu wokhalako musanafike inu.


Potero muzisunga malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, kuwachita; lingakusanzeni inu dziko limene ndipita nanuko, kuti mukhale m'mwemo.


Ndipo asaligulitse dziko chigulitsire; popeza dzikoli ndi langa; pakuti inu ndinu alendo akugonera ndi Ine.


chifukwa chake atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m'mzinda, ndi ana ako aamuna ndi aakazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa chingwe, ndi iwe mwini udzafa m'dziko lodetsedwa; ndipo Israele adzatengedwadi ndende kuchoka m'dziko lake.


Nyamukani, chokani, pakuti popumula panu si pano ai; chifukwa cha udyo wakuononga ndi chionongeko chachikulu.


Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadye ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.


Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.


Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Ejipito ndi ngalawa, panjira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogula inu.


ndiitana kumwamba ndi dziko lapansi zichite mboni pa inu lero lino, kuti mudzaonongeka msangatu kuchotsedwa ku dziko limene muolokera Yordani kulilandira likhale lanulanu; masiku anu sadzachuluka pamenepo, koma mudzaonongeka konse.


Ndipo kudzakhala kuti monga zakugwerani zokoma zonse anakunenerani Yehova Mulungu wanu, momwemo Yehova adzakutengerani zoipa zonse mpaka atakuonongani kukuchotsani m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa