Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 9:4 - Buku Lopatulika

4 Sadzatsanulira Yehova nsembe zavinyo; sizidzamkomera Iye nsembe zao; zidzakhala kwa iwo ngati mkate wa achisoni; onse akudyako adzadetsedwa; pakuti mkate wao udzakhala wa njala yao, uwu sudzalowa m'nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Sadzatsanulira Yehova nsembe zavinyo; sizidzamkomera Iye nsembe zao; zidzakhala kwa iwo ngati mkate wa achisoni; onse akudyako adzadetsedwa; pakuti mkate wao udzakhala wa njala yao, uwu sudzalowa m'nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Kumeneko anthu sadzaperekanso zopereka za chakumwa kupereka kwa Chauta. Sadzamkondwetsanso ndi nsembe zao. Chakudya chao chidzakhala ngati chakudya chapamaliro, onse amene adzadya chakudya chimenecho adzaipitsidwa. Chakudyacho chidzangokhala chodyera njala chabe, osati choti nkukapereka ku Nyumba ya Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Iwo sadzaperekanso chopereka cha chakumwa kwa Yehova, kapena nsembe zawo kuti akondweretse Yehovayo. Nsembe zotere zidzakhala kwa iwo ngati chakudya cha anamfedwa; onse akudya chakudya chimenechi adzakhala odetsedwa. Chakudya ichi chidzakhala chodya okha, sichidzalowa mʼnyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 9:4
33 Mawu Ofanana  

ndi pa mwanawankhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anai la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira.


Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.


Pakuti pa miyala yosalala ya m'chigwa pali gawo lako; iyo ndiyo gawo lako; ndiyo imene unaitsanulirira nsembe yothira, ndi kupereka nsembe yaufa. Kodi ndidzapembedzedwa pa zinthu zimenezi?


Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;


anthu sadzawagawira mkate pamaliro, kuti atonthoze mitima yao chifukwa cha akufa, anthu sadzapatsa iwo chikho cha kutonthoza kuti achimwe chifukwa cha atate ao kapena mai wao.


Lubani andifumiranji ku Sheba, ndi nzimbe ku dziko lakutali? Nsembe zopsereza zanu sizindisekeretsa, nsembe zophera zanu sizindikondweretsa Ine.


Usa moyo mosamveka, usalira wakufayo, dzimangire chilemba, nuvale nsapato kumapazi ako, usaphimbe milomo yako. Kapena kudya mkate wa anthu.


Ndipo mudzachita monga umo ndachitira ine, osaphimba milomo yanu, kapena kudya mkate wa anthu.


Koma Daniele anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya cha mfumu, kapena ndi vinyo amamwa; chifukwa chake anapempha mkulu wa adindo amlole asadzidetse.


Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;


Abwerera, koma si kwa Wam'mwambayo; akunga uta wosakhulupirika; akalonga ao adzagwa ndi lupanga mwa chipongwe cha lilime lao; ichi ndicho adzawasekera m'dziko la Ejipito.


Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukira mphulupulu yao, nadzalanga zochimwa zao; adzabwerera kunka ku Ejipito.


Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.


Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka kunyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, achita maliro.


Kaya, kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pake, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yothira ya Yehova Mulungu wanu.


Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu paguwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake.


Nena ndi Aroni, kuti, Aliyense wa mbeu zako mwa mibadwo yao wakukhala nacho chilema, asayandikize kupereka mkate wa Mulungu wake.


Wa mbeu ya Aroni wansembe asayandikize mmodzi wokhala nacho chilema, kupereka nsembe zamoto za Yehova; ali nacho chilema asayandikize kupereka chakudya cha Mulungu wake.


Azikhala opatulikira Mulungu wao, osaipsa dzina la Mulungu wao; popeza amapereka nsembe zamoto za Yehova, mkate wa Mulungu wao; chifukwa chake akhale opatulika.


Chifukwa chake umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera.


Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndi nsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine.


Ndi ichi mubwereza kuchichita: mukuta guwa la nsembe la Yehova ndi misozi, ndi kulira, ndi kuusa moyo; momwemo Iye sasamaliranso chopereka, kapena kulandira mokondwera m'dzanja lanu.


Iye wakukhudza mtembo wa munthu aliyense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri;


Uza ana a Israele, nuti nao, Muzisamalira kubwera nacho kwa Ine chopereka changa, chakudya changa cha nsembe zanga zamoto, cha fungo lokoma, pa nyengo yake yoikika.


Ndi pa gome la mkate woonekera ayale nsalu yamadzi, naikepo mbale zake, ndi zipande, ndi mitsuko, ndi zikho zakuthira nazo; mkate wa chikhalire uzikhalaponso.


Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. Inde, ndipo mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.


Sindinadyeko m'chisoni changa, kapena kuchotsako podetsedwa, kapena kuperekako kwa akufa; ndamvera mau a Yehova Mulungu wanga; ndachita monga mwa zonse munandilamulira ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa