Chifukwa kuti sanakumbukire kuchita chifundo, koma analondola wozunzika ndi waumphawi, ndi wosweka mtima, kuti awaphe.
Masalimo 10:2 - Buku Lopatulika Podzikuza woipa apsereza waumphawi; agwe m'chiwembu anapanganacho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Podzikuza woipa apsereza waumphawi; agwe m'chiwembu anapanganacho. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu oipa amazunza anthu osauka modzikuza. Akodwe m'misampha yotcha iwo omwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwa kunyada kwake munthu woyipa asaka wofowoka, amene akodwa mʼnjira zimene iye wakonza. |
Chifukwa kuti sanakumbukire kuchita chifundo, koma analondola wozunzika ndi waumphawi, ndi wosweka mtima, kuti awaphe.
Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.
Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.
Pakamwa pao achimwa ndi mau onse a pa milomo yao, potero akodwe m'kudzitamandira kwao, ndiponso chifukwa cha kutemberera ndi bodza azilankhula.
Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkulu ndi milungu yonse, pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa.
Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba paphiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;
Iwo amene akuona iwe adzayang'anitsitsa iwe, nadzalingalira za iwe, ndi kuti, Kodi uyu ndi munthu amene ananthunthumiritsa dziko lapansi, amene anagwedeza maufumu;
pamenepo ananena Azariya mwana wake wa Hosaya, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi anthu onse odzikuza, nati kwa Yeremiya, Unena zonama; Yehova Mulungu wathu sanakutumize iwe kudzanena, Musalowe mu Ejipito kukhala m'menemo;