Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Genesis 5:4 - Buku Lopatulika Masiku ake Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Masiku ake Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Adamu adakhala ndi moyo zaka zinanso 800. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atabadwa Seti, Adamu anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
ndipo anakhala ndi moyo Enosi, atabala Kenani, zaka mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi zisanu: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi.
ndipo Kenani anakhala ndi moyo, atabala Mahalalele zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi anai, ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi;
ndipo Yaredi anakhala ndi moyo, atabala Enoki, zaka mazana asanu ndi atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi;
ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela, zaka mazana atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi;
ndipo Metusela anakhala ndi moyo, atabala Lameki, zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala ana aamuna ndi aakazi:
Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m'chifanizo chake; namutcha dzina lake Seti.
ndipo Lameki anakhala ndi moyo atabala Nowa, zaka mazana asanu kudza makumi asanu ndi anai ndi zisanu, nabala ana aamuna ndi aakazi:
Masiku ake onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anai, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira.
ndipo Seti anakhala ndi moyo, atabala Enosi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza zisanu ndi ziwiri: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi:
Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.
Kuti ana athu aamuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime; ana athu aakazi ngati nsanamira za kungodya, zosema zikometsere nyumba ya mfumu.