Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 5:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m'chifanizo chake; namutcha dzina lake Seti.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m'chifanizo chake; namutcha dzina lake Seti.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Adamu ali wa zaka 130 adabereka mwana wofanafana ndi iye, namutcha Seti.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 5:3
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wake; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Seti, chifukwa anati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu ina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha.


anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nawadalitsa iwo natcha mtundu wao anthu, tsiku lomwe anawalenga iwo.


Masiku ake Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi.


Adzatulutsa choyera m'chinthu chodetsa ndani? Nnena mmodzi yense.


Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu? Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?


Onani, ndinabadwa m'mphulupulu, ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa.


Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.


mwana wa Kainani, mwana wa Arifaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameki,


Chobadwa m'thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu.


Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.


Nyama yonse siili imodzimodzi; koma ina ndi ya anthu, ndi ina ndiyo nyama ya zoweta, ndi ina ndiyo nyama ya mbalame, ndi ina ya nsomba.


Ndipo monga tavala fanizo la wanthakayo, tidzavalanso fanizo la wakumwambayo.


amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa