Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 9:7 - Buku Lopatulika

7 Ndi inu, mubalane, muchuluke; muswane padziko lapansi, nimuchuluke m'menemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndi inu, mubalane, muchuluke; muswane pa dziko lapansi, nimuchuluke m'menemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsopano mubalane, kuti zidzukulu zanu zidzachulukane ndi kudzabalalika pa dziko lonse lapansi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Inu muberekane ndi kuchulukana kuti mudzaze dziko lonse lapansi ndi kuligonjetsa.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 9:7
7 Mawu Ofanana  

Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.


Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, uchuluke; mwa iwe mudzatuluka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzatuluka m'chuuno mwako;


Tulutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse zili ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi; kuti ziswane padziko lapansi, zibalane, zichuluke padziko lapansi.


Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.


Amenewa ndiwo ana aamuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi.


Ndipo Mulungu ananena kwa Nowa ndi kwa ana ake pamodzi naye, kuti,


tengani akazi, balani ana aamuna ndi aakazi; kwatitsani ana anu aamuna, patsani ananu aakazi kwa amuna, kuti abale ana aamuna ndi aakazi; kuti mubalane pamenepo musachepe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa