Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 9:6 - Buku Lopatulika

6 Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 “Aliyense wopha munthu, nayenso adzaphedwa, pakuti munthu adalengedwa muchifaniziro cha Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “Aliyense wopha munthu, adzaphedwanso ndi munthu; pakuti Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 9:6
32 Mawu Ofanana  

Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.


Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanene kwa inu kuti, Musachimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? Chifukwa chakenso, taonani mwazi wake ufunidwa.


Ili ndi buku la mibadwo ya Adamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m'chifanizo cha Mulungu;


Koposa kotani nanga, pamene anthu oipa anapha munthu wolungama pa kama wake m'nyumba yakeyake, ndidzafunsira mwazi wake ku dzanja lanu tsopano, ndi kukuchotsani ku dziko lapansi?


Ndipo tsono, usamuyesera iye wosachimwa, popeza ndiwe munthu wanzeru, ndipo udziwa umo uyenera kumchitira iye, nutsitsire mutu wake waimvi ndi mwazi kumanda.


Pamene Ataliya make wa Ahaziya anaona kuti mwana wake wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yachifumu.


Ndipo anamgwira, napita naye njira yolowera akavalo kunyumba ya mfumu, namupha pomwepo.


Nakondwerera anthu onse a m'dziko, ndi m'mzinda munali phee; ndipo adapha Ataliya ndi lupanga kunyumba ya mfumu.


Ndipo anyamata ake anampangira chiwembu, namupha m'nyumba yakeyake.


Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu; kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.


Wopalamula mlandu wakupha munthu adzathawira kudzenje; asamuletse.


mphindi yakupha ndi mphindi yakuchiza; mphindi yakupasula ndi mphindi yakumanga;


osadza nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti aipereke chopereka cha Yehova, ku bwalo la Kachisi wa Yehova; azimuyesa munthuyu wochimwira mwazi, wakhetsa mwazi; ndipo amsadze munthuyo kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake;


Munthu akakantha munthu mnzake aliyense kuti afe, amuphe ndithu.


Koma akamkantha ndi chipangizo chachitsulo, kuti wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.


ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m'dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere kumzinda wake wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika.


Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko chifukwa cha mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.


Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza lupanga lako m'chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi lupanga.


pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.


Pakuti mwamuna sayenera kuvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.


Koma munthu akamuda mnzake, namlalira, ndi kumuukira ndi kumkantha moyo wake, kuti wafa; nakathawira ku wina wa mizinda iyi;


Timayamika Ambuye ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu;


Ngati munthu alinga kundende, kundende adzamuka; munthu akapha ndi lupanga, ayenera iye kuphedwa nalo lupanga. Pano pali chipiriro ndi chikhulupiriro cha oyera mtima.


Momwemo Mulungu anambwezera Abimeleki choipacho anachitira atate wake ndi kuwapha abale ake makumi asanu ndi awiri.


Ndipo Samuele anati, Monga lupanga lako linachititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samuele anamdula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa