Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova.
Eksodo 5:1 - Buku Lopatulika Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Mose ndi Aroni adapita kwa Farao nakamuuza kuti, “Naŵa mau a Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Uŵalole anthu anga apite ku chipululu, kuti akachite mwambo wachipembedzo wondilemekeza Ine.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ” |
Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova.
Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;
Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akulu athu, ndi ana athu aamuna ndi aakazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tili nao madyerero a Yehova.
Ndipo adzamvera mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israele, kwa mfumu ya Aejipito, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu.
Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu; ndipo penyani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.
Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.
Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake.
Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aejipito, awatulutse ana a Israele mu Ejipito; Mose ndi Aroni amenewa.
Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumikire m'chipululu; koma, taona, sunamvere ndi pano.
Iwe uzilankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkulu wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.
Ndipo anachita chomwecho; pakuti Aroni anasamula dzanja lake ndi ndodo yake, napanda fumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; fumbi lonse lapansi linasanduka nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.
Ndipo Yehova anati kwa Mose Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; taona, atuluka kunka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire.
Timuke ulendo wa masiku atatu m'chipululu, tikamphere Yehova Mulungu wathu nsembe, monga adzanena nafe.
Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, numuuze, Atero Yehova Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.
Ndipo m'phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.
Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu iwe, usawaopa, kapena kuopa mau ao; ingakhale mitungwi ndi minga ikhala ndi iwe, nukhala pakati pa zinkhanira, usaopa mau ao kapena kuopsedwa ndi nkhope zao; pakuti ndiwo nyumba yopanduka.
ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.
Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.
Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse,
chifukwa chake tichita phwando, si ndi chotupitsa chakale, kapena ndi chotupitsa cha dumbo, ndi kuipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuona mtima, ndi choonadi.