Eksodo 10:9 - Buku Lopatulika9 Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akulu athu, ndi ana athu aamuna ndi aakazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tili nao madyerero a Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akulu athu, ndi ana athu aamuna ndi aakazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tili nao madyerero a Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Mose adayankha kuti, “Tidzapita tonse ndi ana athu, pamodzi ndi nkhalamba zathu zomwe. Tidzapita ndi ana aamuna, ana aakazi, nkhosa zathu ndi mbuzi zomwe. Tidzatenganso ndi ng'ombe zomwe, chifukwa choti tikachita mwambo wachipembedzo wolemekeza Chauta.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Mose anayankha kuti, “Ife tidzapita tonse pamodzi; angʼonoangʼono ndi akuluakulu, ana athu aamuna ndi aakazi, ndiponso ziweto zathu ndi ngʼombe chifukwa tikakhala ndi chikondwerero cha kwa Yehova.” Onani mutuwo |