Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 8:27 - Buku Lopatulika

27 Timuke ulendo wa masiku atatu m'chipululu, tikamphere Yehova Mulungu wathu nsembe, monga adzanena nafe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Timuke ulendo wa masiku atatu m'chipululu, tikamphere Yehova Mulungu wathu nsembe, monga adzanena nafe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Tiyenera kuyenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wathu, monga adatilamulira.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Ife tiyenera kuyenda ulendo wa masiku atatu kupita ku chipululu kukapereka nsembe kwa Yehova Mulungu wathu monga anatilamulira.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 8:27
8 Mawu Ofanana  

Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.


Ndipo Iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo mu Ejipito, mudzatumikira Mulungu paphiri pano.


Ndipo adzamvera mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israele, kwa mfumu ya Aejipito, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu.


Dzisungire chimene Ine ndikuuza lero lino: taona, ndiingitsa pamaso pako Aamori ndi Akanani, ndi Ahiti ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.


Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu.


Ndipo iwo anati, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; timuketu ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kumphera nsembe Yehova Mulungu wathu; kuti angatikanthe ndi mliri, kapena ndi lupanga.


Ndipo ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu anatenga yense mbale yake ya zofukiza, naikamo moto, naikapo chofukiza, nabwera nao pamaso pa Yehova moto wachilendo, umene sanawauze.


ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa