Eksodo 4:31 - Buku Lopatulika Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israele, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israele, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Aisraele aja adakhulupiriradi zimenezo. Tsono atamva kuti Chauta adadzaŵayendera ndipo kuti adaona kuzunzika kwaoko, adaŵeramitsa mitu pansi napembedza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anakhulupirira. Iwo atamva kuti Yehova anadzawayendera ndi kuti waona mmene akuzunzikira, anaweramitsa mitu pansi napembedza. |
Ndipo Leya anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Rubeni; pakuti anati, Chifukwa kuti Yehova waona kuvutika kwanga ndipo tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine.
Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.
Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.
Ndipo Yehosafati anawerama mutu wake, nkhope yake pansi; ndi Ayuda onse, ndi okhala mu Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova.
pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anachirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.
Ndi ana onse a Israele anapenyerera potsika motowo, ndi pokhala ulemerero wa Yehova pa nyumbayi; nawerama nkhope zao pansi poyalidwa miyala, nalambira, nayamika Yehova, nati, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire.
Pamenepo Ezara analemekeza Yehova Mulungu wamkulu. Navomereza anthu onse, ndi kuti, Amen, Amen; nakweza manja ao, nawerama, nalambira Yehova nkhope zao pansi.
Pamenepo Yobu ananyamuka, nang'amba malaya ake, nameta mutu wake, nagwa pansi, nalambira,
Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele mu Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu.
Ndipo Israele anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aejipito, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.
Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akuvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.
Muka, nukasonkhanitse akulu a Israele, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndakuzondani ndithu, ndi kuona chomwe akuchitirani mu Ejipito;
Ndipo adzamvera mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israele, kwa mfumu ya Aejipito, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu.
Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;
Ndipo anthu onse anaona mtambo njo ulikuima pakhomo pa chihema; ndi anthu onse anaimirira, nalambira, yense pakhomo pa hema wake.
kuti akhulupirire kuti wakuonekera Yehova Mulungu wa makolo ao, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo.
Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala la otsala a nyumba ya Yuda; adzadyetsa zoweta zao pamenepo; madzulo adzagona m'nyumba za Asikeloni; pakuti Yehova Mulungu wao adzawazonda, nadzabweza undende wao.
Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.
Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.
Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ake kuti abwerere kuchoka m'dziko la Mowabu; pakuti adamva m'dziko la Mowabu kuti Yehova adasamalira anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.