Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 8:6 - Buku Lopatulika

6 Pamenepo Ezara analemekeza Yehova Mulungu wamkulu. Navomereza anthu onse, ndi kuti, Amen, Amen; nakweza manja ao, nawerama, nalambira Yehova nkhope zao pansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Pamenepo Ezara analemekeza Yehova Mulungu wamkulu. Navomereza anthu onse, ndi kuti, Amen, Amen; nakweza manja ao, nawerama, nalambira Yehova nkhope zao pansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Kenaka Ezara adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wamkulu!” Ndipo anthu onse adakweza manja nayankha kuti, “Inde momwemo, inde momwemo.” Pambuyo pake adaŵeramitsa mitu pansi ndipo adapembedza Chauta ali chizyolikire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ezara anatamanda Yehova, Mulungu wamkulu, ndipo anthu onse anakweza manja awo ndi kuyankha kuti, “Ameni, ameni.” Pambuyo pake onse anaweramitsa pansi mitu yawo napembedza Yehova akanali chizolikire choncho.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 8:6
30 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi


Munthuyo ndipo anawerama mutu namyamika Yehova.


Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndipo anthu onse anati, Amen! Nalemekeza Yehova.


Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israele, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.


Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.


Ndipo Yehosafati anawerama mutu wake, nkhope yake pansi; ndi Ayuda onse, ndi okhala mu Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova.


Tsono mumtima mwanga nditi ndichite chipangano ndi Yehova Mulungu wa Israele, kuti mkwiyo wake waukali utembenuke kutichokera.


Hezekiya mfumu ndi akalonga nauzanso Alevi aimbire Yehova zomlemekeza ndi mau a Davide ndi a Asafu mlauli. Ndipo anaimbira zomlemekeza mokondwera, nawerama mitu yao, nalambira.


Nati iye, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, wakunena m'kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi manja ake, ndi kuti,


Ndinakutumulanso malaya anga, ndi kuti, Mulungu akutumule momwemo munthu yense wosasunga mau awa, kunyumba yake, ndi kuntchito yake; inde amkutumule momwemo, namtayire zake zonse. Ndi msonkhano wonse unati, Amen, nalemekeza Yehova. Ndipo anthu anachita monga mwa mau awa.


Ndi Yesuwa, ndi Bani, ndi Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseiya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani, Pelaya, ndi Alevi, anadziwitsa anthu chilamulocho; ndi anthu anali chilili pamalo pao.


Kwezani manja anu kumalo oyera, nimulemekeze Yehova.


Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.


Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu, pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.


Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen.


Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga; ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.


Pakuti Yehova ndiye Mulungu wamkulu; ndi mfumu yaikulu yoposa milungu yonse.


Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele mu Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu.


Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israele, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu.


Yeremiya mneneri anati, Amen: Yehova achite chotero: Yehova atsimikize mau ako amene wanenera, abwezerenso zipangizo za nyumba ya Yehova, ndi onse amene anachotsedwa am'nsinga, kuchokera ku Babiloni kudza kumalo kuno.


Titukulire mitima yathu ndi manja athu omwe kwa Mulungu ali kumwamba.


Ndipo unatuluka moto pamaso ya Yehova, nunyeketsa nsembe yopsereza ndi mafuta paguwa la nsembe; ndipo pakuchiona anthu onse anafuula, nagwa nkhope zao pansi.


Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.


Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.


Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena?


Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;


Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.


Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;


Ndipo angelo onse anaimirira pozinga mpando wachifumu, ndi akulu, ndi zamoyozo zinai; ndipo anagwa nkhope yao pansi kumpando wachifumu, nalambira Mulungu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa