Nehemiya 8:5 - Buku Lopatulika5 Ndipo Ezara anafunyulula bukulo pamaso pa anthu onse, popeza iye anasomphokera anthu onse; ndipo polifunyulula anthu onse ananyamuka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo Ezara anafunyulula bukulo pamaso pa anthu onse, popeza iye anasomphokera anthu onse; ndipo polifunyulula anthu onse ananyamuka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Tsono ataimirira pansanjapo, Ezara adafutukula buku, anthu onse akupenya. Pomwepo anthu onse adaimirira. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Tsono Ezara anatsekula buku, akuona popeza anayima pa nsanja. Pamene anafutukula bukulo anthu onse anayimirira. Onani mutuwo |
Ndipo Ezara mlembi anaima pa chiunda cha mitengo adachimangira msonkhanowo; ndi pambali pake padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseiya, kudzanja lamanja lake; ndi kudzanja lamanzere Pedaya, ndi Misaele, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.