Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 3:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m'Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Kenaka Chauta adati, “Ndaona m'mene anthu anga akuzunzikira ku Ejipito. Ndamva kulira kwao kofuna chithandizo, chifukwa cha anthu amene akuŵapsinja. Ndikudziŵa bwino kuzunzika kwao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Yehova anati, “Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo chifukwa cha anthu amene akuwapsinja, ndipo ndakhudzidwa ndi masautso awo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 3:7
31 Mawu Ofanana  

Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamutcha dzina lake Ismaele; chifukwa Yehova anamva kusauka kwako.


ndidzatsikatu ndikaone ngati anachita monse monga kulira kwake kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziwa.


Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? Usaope; chifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.


Ndipo Leya anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Rubeni; pakuti anati, Chifukwa kuti Yehova waona kuvutika kwanga ndipo tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine.


Ndipo anati, Tukulatu maso ako, nuone, atonde onse amene akwera zoweta ali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga: chifukwa ndaona zonse zimene Labani akuchitira iwe.


Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.


Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa; koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwachepetse.


Koma Yehowahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwake kwa Israele m'mene mfumu ya Aramu inawapsinja.


Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova.


Ndipo munapenya msauko wa makolo athu mu Ejipito, nimunamva kufuula kwao ku Nyanja Yofiira,


Koma anapenya nsautso yao, pakumva kufuula kwao:


Mau a Yehova ndi mau oona; ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi, yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.


Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.


Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.


Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.


Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m'mantha anga onse.


Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.


Yehova, mudazipenya; musakhale chete, Ambuye, musakhale kutali ndi ine.


Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu.


Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.


Pamenepo inalowa mfumu yatsopano mu ufumu wa Ejipito, imene siinadziwe Yosefe.


Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang'ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwao;


Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu; ndipo penyani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.


Ndipo akufulumiza anthu ndi akapitao ao anatuluka, nanena ndi anthu ndi kuti, Atero Farao, Kulibe kukupatsani udzu.


Ndipo tsiku lomwelo Farao analamulira akufulumiza anthu, ndi akapitao ao, ndi kuti,


M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.


Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natitulutsa mu Ejipito; ndipo, taonani, tili mu Kadesi, ndiwo mzinda wa malekezero a malire anu.


Kuona ndaona choipidwa nacho anthu anga ali mu Ejipito, ndipo amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano, tiye kuno, ndikutume ku Ejipito.


Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.


Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israele, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa