Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 3:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Yehova anati, “Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo chifukwa cha anthu amene akuwapsinja, ndipo ndakhudzidwa ndi masautso awo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m'Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Kenaka Chauta adati, “Ndaona m'mene anthu anga akuzunzikira ku Ejipito. Ndamva kulira kwao kofuna chithandizo, chifukwa cha anthu amene akuŵapsinja. Ndikudziŵa bwino kuzunzika kwao.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 3:7
31 Mawu Ofanana  

Mngelo wa Yehova uja anamuwuzanso kuti, “Ndiwe woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna. Udzamutcha dzina lake Ismaeli, pakuti Yehova wamva kulira chifukwa cha kuzunzika kwako.


choncho ndikuti ndipiteko ndikaone ngati zimene achita zilidi zoyipa monga mmene madandawulo andipezera Ine. Ngati sizili choncho, ndikadziwa.”


Mulungu anamva mnyamatayo akulira ndipo mngelo wa Mulungu anayankhula kwa Hagara kuchokera kumwamba nati, “Chavuta nʼchiyani Hagara? Usachite mantha; Mulungu wamva kulira kwa mnyamatayo pamene wagonapo.


Leya anakhala ndi pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha Rubeni pakuti anati, “Yehova waona kusauka kwanga. Zoonadi, mwamuna wanga adzandikonda tsopano.”


Ndipo iye anati, ‘Tayangʼana ndipo taona kuti atonde onse okwerana ndi ziweto ali amichocholozi, amawangamawanga kapena a mathothomathotho, popeza ndaona zonse zimene Labani wakhala akukuchitira.


Akanapanda kukhala nane Mulungu wa abambo anga, Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu amene Isake ankamuopa, mosakayika inu mukanandichotsa chimanjamanja. Koma Mulungu waona zovuta zanga ndi kulimbikira ntchito kwanga, ndipo usiku wapitawu anakudzudzulani.”


Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa, koma maso anu amatsutsana ndi odzikuza ndipo mumawatsitsa.


Tsono Yehowahazi anapempha Yehova kuti amuchitire chifundo ndipo Yehova anamva pempho lake chifukwa anaona momwe mfumu ya Aramu inkapsinjira Aisraeli.


“Bwerera, kamuwuze Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona ndipo ndidzakuchiritsa. Tsiku lachitatu kuchokera lero udzapita ku Nyumba ya Yehova.


“Munaona kuzunzika kwa makolo athu ku Igupto. Munamva kufuwula kwawo pa Nyanja Yofiira.


Koma Iye anaona kuzunzika kwawo pamene anamva kulira kwawo;


Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi, oyengedwa kasanu nʼkawiri.


Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga, ndinu amene mudziwa njira yanga. Mʼnjira imene ndimayendamo anthu anditchera msampha mobisa.


Iye amakwaniritsa zokhumba za iwo amene amamuopa; amamva kulira kwawo ndi kuwapulumutsa.


Pakuti Iye sanapeputse kapena kunyoza kuvutika kwa wosautsidwayo; Iye sanabise nkhope yake kwa iye. Koma anamvera kulira kwake kofuna thandizo.


Ine ndinafunafuna Yehova ndipo Iye anandiyankha; anandilanditsa ku mantha anga onse.


Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva; Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse.


Yehova mwaona zimenezi; musakhale chete. Ambuye musakhale kutali ndi ine.


kuti ndilengeze za matamando anu pa zipata za ana aakazi a Ziyoni, kuti pamenepo ndikondwere ndi chipulumutso chanu.


Kotero anayika akapitawo kuti aziwazunza ndi kuwagwiritsa ntchito yolemetsa mokakamiza. Iwo anamangira Farao mizinda ya Pitomu ndi Ramesesi kumene ankasungirako chakudya.


Pambuyo pake mfumu yatsopano imene sinkamudziwa Yosefe, inayamba kulamulira dziko la Igupto.


Ngati muwazunza ndipo iwo nʼkulirira kwa Ine, ndidzamva kulira kwawo.


Ngati mwakondwera nane ndiphunzitseni njira zanu kuti ndikudziweni ndi kupitiriza kupeza chisomo pamaso panu. Kumbukirani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.”


Choncho akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu anapita kwa anthu aja nati, “ ‘Farao akuti sadzakupatsaninso udzu.


Pa tsiku lomwelo Farao analamulira akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu kuti


Iyenso anasautsidwa mʼmasautso awo onse, ndipo mngelo wochokera kwa Iye anawapulumutsa. Mwa chikondi ndi chifundo chake iye anawapulumutsa, anawanyamula ndikuwatenga kuyambira kale lomwe.


koma titalirira Yehova, Iyeyo anamva kulira kwathuko ndipo anatitumizira mngelo amene anatitulutsa ku Igupto.” “Taonani, tsopano tili pano pa Kadesi, mzinda wa mʼmalire a dziko lanu.


Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo choncho ndabwera kuti ndiwapulumutse. Tsopano tiye ndikutume ku Igupto.’


Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe.


“Mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini. Udzamudzoze kuti akhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli. Iye adzawapulumutsa mʼdzanja la Afilisti. Ine ndaona kuzunzika kwawo ndipo ndamva kulira kwawo.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa