Kapena Yehova adzayang'anira chosayenerachi alikundichitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera chabwino m'malo mwa kunditukwana kwa lero.
Eksodo 2:25 - Buku Lopatulika Ndipo Mulungu anapenya Aisraele, ndi Mulungu anadziwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mulungu anapenya Aisraele, ndi Mulungu anadziwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu ataŵapenya Aisraelewo, adaŵamvera chifundo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu ataona Aisraeli aja ndi masautso awo, Iye anawamvera chifundo. |
Kapena Yehova adzayang'anira chosayenerachi alikundichitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera chabwino m'malo mwa kunditukwana kwa lero.
Apenyerera anthu, ndi kuti, ndinachimwa, ndaipsa choongokacho, ndipo sindinapindule nako.
Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.
Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.
Ndipo Mose anafotokozera mpongozi wake zonse Yehova adazichitira Farao ndi Aejipito chifukwa cha Israele; ndi mavuto onse anakomana nao panjira, ndi kuti Yehova adawalanditsa.
Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israele kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aejipito awapsinja nako.
Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israele, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu.
Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziweni inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.
Ambuye wandichitira chotero m'masiku omwe Iye anandipenyera, kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.
Kuona ndaona choipidwa nacho anthu anga ali mu Ejipito, ndipo amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano, tiye kuno, ndikutume ku Ejipito.
Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, Mulungu wa makolo athu; ndipo Yehova anamva mau athu, napenya kuzunzika kwathu, ndi ntchito yathu yolemetsa, ndi kupsinjika kwathu;
nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.