Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 31:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo simunandipereke m'dzanja la mdani; munapondetsa mapazi anga pali malo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo simunandipereka m'dzanja la mdani; munapondetsa mapazi anga pali malo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Simudandipereke m'manja mwa adani anga, koma mwandiika pa malo otambalala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Inu simunandipereke kwa mdani koma mwayika mapazi anga pa malo otakasuka.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 31:8
13 Mawu Ofanana  

Mulungu andipereka kwa osulangama, nandiponya m'manja a oipa.


Inde akadakukopani muchoke posaukira, mulowe kuchitando kopanda chopsinja; ndipo zoikidwa pagome panu zikadakhala zonona ndithu.


Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.


Ananditulutsanso andifikitse motakasuka; anandilanditsa, pakuti anakondwera ndi ine.


Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.


Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali; munandiika ndiwakhalire chonyansa. Ananditsekereza, osakhoza kutuluka ine.


Ndipo Mulungu anapenya Aisraele, ndi Mulungu anadziwa.


Ndipo ndidzapereka Ejipito m'manja mwa mbuye wankharwe; ndi mfumu yaukali idzawalamulira, ati Ambuye, Yehova wa makamu.


Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, Mulungu wa makolo athu; ndipo Yehova anamva mau athu, napenya kuzunzika kwathu, ndi ntchito yathu yolemetsa, ndi kupsinjika kwathu;


Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.


Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu.


Ndipo unatsimikiza lero lino kuti wandichitira zabwino; chifukwa sunandiphe pamene Yehova anandipereka m'dzanja lako.


Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m'dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa