Eksodo 11:5 - Buku Lopatulika ndipo ana oyamba a m'dziko la Ejipito adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wachifumu wake, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo ana oyamba a m'dziko la Ejipito adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wachifumu wake, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo mwana aliyense wachisamba adzaphedwa mu Ejipito monse muno. Kuyambira mwana wachisamba wa Farao, amene ali woyenera kuloŵa ufumu, adzaphedwa, mpaka mwana wachisamba wa mdzakazi amene akupera pa mphero. Mwana woyamba kubadwa wa zoŵeta adzafanso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mwana aliyense wamwamuna wachisamba adzafa, kuyambira mwana wamwamuna wa Farao amene amakhala pa mpando waufumu, mpaka mwana wamwamuna wachisamba wa mdzakazi wake amene ali naye pa mtondo, komanso ana oyamba a ziweto. |
Pakuti ndidzapita pakati padziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova.
Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m'dziko la Ejipito, kuyambira mwana woyamba wa Farao wakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam'nsinga ali m'kaidi; ndi ana oyamba onse a zoweta.
ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; chifukwa chake ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola.
Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.
Tenga mipero, nupere ufa; chotsa chophimba chako, vula chofunda, kwinda m'mwendo, oloka mitsinje.
Ndi chikhulupiriro anachita Paska, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuononga ana oyamba angawakhudze iwo.
Pamenepo Afilisti anamgwira, namkolowola maso, natsika naye ku Gaza, nammanga ndi maunyolo amkuwa; namperetsa m'kaidi.