Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 11:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndipo mwana aliyense wamwamuna wachisamba adzafa, kuyambira mwana wamwamuna wa Farao amene amakhala pa mpando waufumu, mpaka mwana wamwamuna wachisamba wa mdzakazi wake amene ali naye pa mtondo, komanso ana oyamba a ziweto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 ndipo ana oyamba a m'dziko la Ejipito adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wachifumu wake, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 ndipo ana oyamba a m'dziko la Ejipito adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wachifumu wake, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 ndipo mwana aliyense wachisamba adzaphedwa mu Ejipito monse muno. Kuyambira mwana wachisamba wa Farao, amene ali woyenera kuloŵa ufumu, adzaphedwa, mpaka mwana wachisamba wa mdzakazi amene akupera pa mphero. Mwana woyamba kubadwa wa zoŵeta adzafanso.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 11:5
13 Mawu Ofanana  

Kenaka anakantha ana onse oyamba kubadwa a mʼdziko lawo, zipatso zoyamba za umunthu wawo wonse.


Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto, ana oyamba kubadwa a anthu ndi nyama.


Amene anakantha ana woyamba kubadwa a Igupto, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.


Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto, zipatso zoyamba kucha za mphamvu zawo mʼmatenti a Hamu


“Usiku umenewo Ine ndidzadutsa mʼdziko la Igupto ndipo ndidzapha chilichonse choyamba kubadwa kuyambira mwana wa munthu aliyense mpaka ana aziweto. Ndidzalanganso milungu yonse ya Igupto. Ine ndine Yehova.


Pakati pa usiku Yehova anakantha ana onse oyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira woyamba kubadwa wa Farao, amene amakhala pa mpando waufumu wa Faraoyo, mpaka mwana woyamba kubadwa wa munthu amene anali mʼdzenje, pamodzinso ndi ana oyamba kubadwa a ziweto zawo.


Farao atakanitsitsa kuti asatitulutse, Yehova anapha aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira ana a anthu ndi ziweto zomwe. Nʼchifukwa chake ine ndimapereka nsembe kwa Yehova, chachimuna chilichonse choyamba kubadwa ndipo mwana wamwamuna woyamba kubadwa ndimamuwombola.’


Choncho ndikuti, ‘Mulole mwana wanga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana, Ine ndidzapha mwana wako wachisamba.’ ”


Tenga mphero ndipo upere ufa; chotsa nsalu yako yophimba nkhope kwinya chovala chako mpaka ntchafu ndipo woloka mitsinje.


Achinyamata akukakamizidwa kupera tirigu; anyamata akudzandira ndi mitolo ya nkhuni.


Amayi awiri adzakhala akusinja pa mtondo; wina adzatengedwa ndi wina adzatsala.


Ndi chikhulupiriro anachita Paska ndi kuwaza magazi, kuti mngelo wowononga ana oyamba kubadwa asaphe ana oyamba kubadwa a Aisraeli.


Afilisti anamugwira ndipo anamukolowola maso. Kenaka anapita naye ku Gaza atamumanga ndi maunyolo achitsulo. Kumeneko anakhala wa pamphero mu ndende.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa