Danieli 2:23 - Buku Lopatulika Ndikuyamikani ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mphamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano ichi tachifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndikuyamikani ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mphamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano ichi tachifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikuyamika ndi kutamanda Inu Mulungu wa makolo anga: mwandipatsa nzeru ndi mphamvu, mwandiwululira zomwe tinakupemphani, mwatiwululira maloto a mfumu.” |
Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.
Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isaki ndi Israele, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israele, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndachita zonsezi.
Yehova Mulungu wathu akhale nafe monga umo anakhalira nao makolo athu, asatisiye kapena kutitaya;
Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israele, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.
nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa mu Mwamba kodi? Sindinu woweruza maufumu onse a amitundu kodi? Ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulimbana ndi Inu.
Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m'mibadwomibadwo.
Pamenepo ndinati, Nzeru ipambana mphamvu; koma anyoza nzeru ya wosauka, osamvera mau ake.
Tsiku lomwelo udzati, Ndikuyamikani inu Yehova; pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mutonthoza mtima wanga.
Undiitane Ine, ndipo Ine ndidzakuyankha iwe, ndipo ndidzakusonyeza iwe zazikulu, ndi zopambana, zimene suzidziwa.
Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.
kuti apemphe zachifundo kwa Mulungu wa Kumwamba pa chinsinsi ichi; kuti Daniele ndi anzake asaonongeke pamodzi ndi eni nzeru ena a ku Babiloni.
Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.
Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:
Nthawi yomweyo Iye anakondwera ndi Mzimu Woyera, nati, Ndikuvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu.
Pomwepo anachotsa mwala. Koma Yesu anakweza maso ake kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.
Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.
Chivumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane;
ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana kuti akhoza kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.