Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 31:42 - Buku Lopatulika

42 Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Mulungu wa atate anga, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu amene Isaki ankamuwopa, akadapanda kukhala nane, bwenzi mutandichotsa kale ndili chimanjamanja. Koma Mulungu adaona mavuto anga ndi ntchito za manja anga, ndipo usiku wapitawu Iye wakutsutsani.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Akanapanda kukhala nane Mulungu wa abambo anga, Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu amene Isake ankamuopa, mosakayika inu mukanandichotsa chimanjamanja. Koma Mulungu waona zovuta zanga ndi kulimbikira ntchito kwanga, ndipo usiku wapitawu anakudzudzulani.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:42
22 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anatsikira kudzaona mzinda ndi nsanja imene analinkumanga ana a anthu.


Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamutcha dzina lake Ismaele; chifukwa Yehova anamva kusauka kwako.


Ndipo anatcha dzina la Yehova amene ananena naye, Ndinu Mulungu wakundiona ine; pakuti anati, Kodi kunonso ndayang'ana pambuyo pake pa Iye amene wakundiona ine?


Ndipo Isaki ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukulu, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadalowe iwe, ndipo ndamdalitsa iye? Inde, adzadalitsika.


Ndipo Leya anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Rubeni; pakuti anati, Chifukwa kuti Yehova waona kuvutika kwanga ndipo tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine.


Ndipo anati, Tukulatu maso ako, nuone, atonde onse amene akwera zoweta ali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga: chifukwa ndaona zonse zimene Labani akuchitira iwe.


Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.


M'dzanja langa muli mphamvu yakuchitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.


ndipo anati kwa iwo, Ndiona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekere ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine.


Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wao aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wake Isaki.


Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isaki, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira iwe bwino:


tinyamuke, tikwere tinke ku Betele: ndipo tidzamanga kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anandivomereza tsiku la mavuto anga, ndiponso anali ndi ine m'njira m'mene ndinapitamo.


Ndipo Israele anamuka ulendo wake ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isaki atate wake.


Ndipo Davide anatuluka kukomana nao, nayankha, nanena nao, Ngati mwandidzera mwamtendere kundithandiza, mtima wanga udzalumikizana nanu; koma ngati mwafika kundipereka kwa adani anga, popeza m'manja mwanga mulibe chiwawa, Mulungu wa makolo athu achione ndi kuchilanga.


Ndidzakondwera ndi kusangalala m'chifundo chanu, pakuti mudapenya zunzo langa; ndipo mudadziwa mzimu wanga mu nsautso yanga.


Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;


Yehova wa makamu, Iye mudzamyeretsa; muope Iye, akuchititseni mantha Iye.


Ndikuyamikani ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mphamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano ichi tachifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu.


Ndipo pomlola iwe achoke kwanu waufulu, musamamlola achoke wopanda kanthu;


Koma Mikaele mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbike mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa