Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 5:5 - Buku Lopatulika

5 ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana kuti akhoza kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu wa Davide, walakika kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Apo mmodzi mwa Akuluakulu aja adandiwuza kuti, “Usalire, pakuti Mkango wa m'fuko la Yuda, chidzukulu cha mfumu Davide, wapambana, ndipo Iye angathe kufutukula bukulo ndi kumatula zimatiro zake zisanu ndi ziŵiri zija.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Tsono mmodzi mwa akuluakulu aja anati kwa ine, “Usalire! Taona, Mkango wa fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana. Iye angathe kufutukula bukuli ndi kumatula zomatira zisanu ndi ziwirizo.”

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 5:5
25 Mawu Ofanana  

Ndipo anaimika mikango khumi ndi iwiri mbali ina ndi ina, pa makwerero asanu ndi limodzi aja; m'dziko lililonse lina simunapangidwe wotere.


Ndi mpando wachifumuwo unali nao makwerero asanu ndi limodzi, ndi chopondapo mapazi chagolide, omangika ku mpandowo; ndi ku mbali zonse ziwiri za pokhalirapo kunali manja; ndi mikango iwiri inaimirira m'mbali mwa manjawo.


Mamba ake olimba ndiwo kudzitama kwake; amangika pamodzi ngati okomeredwatu.


Ndipo padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese, ndi nthambi yotuluka m'mizu yake idzabala zipatso;


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.


Yehova atero: Letsa mau ako asalire, ndi maso anu asagwe misozi; pakuti ntchito yako idzalandira mphotho, ati Yehova; ndipo adzabweranso kuchokera kudziko la mdani.


Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za choonadi za ichi chonse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwake kwa zinthuzi:


Anaunthama, nagona pansi ngati mkango, ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani? Wodalitsika aliyense wakudalitsa iwe, wotemberereka aliyense wakutemberera iwe.


Koma Yesu anawapotolokera nati, Ana aakazi inu a Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu.


Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.


Ndipo anthu onse analikumlira iye ndi kudziguguda pachifuwa. Koma Iye anati, Musalire; pakuti iye sanafe, koma wagona tulo.


Ndipo iwowa ananena kwa iye, Mkazi, uliranji? Ananena nao, Chifukwa anachotsa Ambuye wanga, ndipo sindidziwa kumene anamuika Iye.


wakunena za Mwana wake, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi,


Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Yese, ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.


Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhule kanthu ka ansembe.


Chivumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane;


Ine Yesu ndatuma mngelo wanga kukuchitirani umboni za izi mu Mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda.


Iye wakupambana, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinapambana, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.


akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, namlambira Iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao kumpando wachifumu, ndi kunena,


Ndipo pozinga mpando wachifumu mipando yachifumu makumi awiri mphambu inai, ndipo pa mipandoyo padakhala akulu makumi awiri mphambu anai, atavala zovala zoyera, ndi pamitu pao akorona agolide.


Ndipo ndinalira kwambiri, chifukwa sanapezeke mmodzi woyenera kutsegula bukulo, kapena kulipenya;


Ndipo ndinaona pamene Mwanawankhosa anamasula chimodzi cha zizindikiro zisanu ndi ziwiri, ndipo ndinamva chimodzi mwa zamoyo zinai, chikunena, ngati mau a bingu, Idza.


Ndipo mmodzi wa akulu anayankha, nanena ndi ine, Iwo ovala zovala zoyera ndiwo ayani, ndipo achokera kuti?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa