taona, ndachita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka.
Danieli 1:17 - Buku Lopatulika Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kwa anyamata anayiwa Mulungu anapereka chidziwitso ndi kuzindikira bwino mitundu yonse ya zolembedwa ndi za maphunziro. Ndipo Danieli ankatanthauzira masomphenya ndi maloto a mitundu yonse. |
taona, ndachita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka.
Ndipo Aisraele onse anamva maweruzidwe ake idaweruza mfumu, naopa mfumu; pokhala anaona kuti nzeru ya Mulungu inali mwa iye yakuweruza.
Mundipatse tsono nzeru ndi chidziwitso, kuti ndituluke ndi kulowa pamaso pa anthu awa; pakuti angathe ndani kuweruza anthu anu awa ambiri?
nzeru ndi chidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso chuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhale nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.
Ndipo iye anali munthu wakufuna Mulungu masiku a Zekariya, ndiye wozindikira masomphenya a Mulungu; ndipo masiku akufunira Yehova iye, Mulungu anamlemereza;
Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Atatha masiku inanenawo mfumu kuti alowe nao, mkulu wa adindo analowa nao pamaso pa Nebukadinezara.
Ndipo m'mau ali onse anzeru ndi aluntha, amene mfumu inawafunsira. Inawapeza akuposa alembi ndi openda onse mu ufumu wake wonse.
anyamata opanda chilema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ochenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'chinyumba cha mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Ababiloni.
Chaka chachitatu cha Kirusi mfumu ya Persiya, chinavumbulutsidwa chinthu kwa Daniele, amene anamutcha Belitesazara; ndipo chinthucho nchoona, ndicho nkhondo yaikulu; ndipo anazindikira chinthucho, nadziwa masomphenyawo.
Pamenepo chinsinsicho chinavumbulutsidwa kwa Daniele m'masomphenya a usiku. Ndipo Daniele analemekeza Mulungu wa Kumwamba.
pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira.
Ndikuyamikani ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mphamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano ichi tachifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu.
Koma ine, chinsinsi ichi sichinavumbulutsidwe kwa ine chifukwa cha nzeru ndili nayo yakuposa wina aliyense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu.
Chifukwa chake ndinalamulira kuti adze kwa ine anzeru onse a ku Babiloni, kuti andidziwitse kumasulira kwake kwa lotoli.
Ndamva za iwe kuti muli mzimu wa milungu mwa iwe, ndi kuti mupezeka mwa iwe kuunika, ndi luntha, ndi nzeru zopambana.
Chaka choyamba cha Belisazara mfumu ya ku Babiloni Daniele anaona loto, naona masomphenya a m'mtima mwake pakama pake; ndipo analemba lotolo, nalifotokozera, mwachidule.
Chaka chachitatu cha Belisazara mfumu masomphenya anandionekera kwa ine Daniele, atatha kundionekera oyamba aja.
Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.
Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.
namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse.
Ndipo Mose anaphunzira nzeru zonse za Aejipito; nali wamphamvu m'mau ake ndi m'ntchito zake.
Mwa ichi ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziwitso cha mzimu,
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.