Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 1:17 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Kwa anyamata anayiwa Mulungu anapereka chidziwitso ndi kuzindikira bwino mitundu yonse ya zolembedwa ndi za maphunziro. Ndipo Danieli ankatanthauzira masomphenya ndi maloto a mitundu yonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

17 Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 1:17
36 Mawu Ofanana  

Ine ndidzakuchitira zimene wapempha. Ndidzakupatsa mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu, kotero kuti sipanakhalepo wina wofanana nawe ndipo sipadzapezekanso wina wonga iwe pambuyo pako.


Pamene Aisraeli onse anamva za chigamulo chimene mfumu inapereka, anaopa mfumuyo kwambiri, chifukwa anaona kuti mfumu inali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu zoweruzira mwachilungamo.


Mundipatse nzeru ndi luntha zolamulira anthu awa, pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”


Ine ndidzakupatsa nzeru ndi chidziwitso. Ndipo ndidzakupatsanso katundu, chuma ndi ulemu, zinthu zoti palibe mfumu imene inali nazo iwe usanakhalepo ndipo palibe wina amene adzakhale nazo iweyo ukadzafa.”


Iye anapembedza Mulungu nthawi ya Zekariya, amene ankamulangiza za kuopa Mulungu amene anamupatsa chipambano.


Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu, mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu.


Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru, ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.


Munthu amene amakondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamusandutsa wanzeru, wozindikira ndi wachisangalalo, koma wochimwa, Mulungu amamupatsa ntchito yosonkhanitsa ndi kusunga chuma kuti adzachipereke kwa amene Mulunguyo amakondwera naye. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.


Mulungu wake amamulangiza ndi kumuphunzitsa njira yabwino.


Taona, ndiwedi wanzeru kupambana Danieli. Ndipo palibe chinsinsi chobisika kwa iwe.


Ndipo kumapeto kwa masiku amene mfumu inayika kuti adzaonetse anyamatawa ku nyumba yake, mkulu wa nduna za mfumu uja anawapereka iwo kwa Nebukadinezara.


Nthawi zonse mfumu ikawafunsa zonse zofuna nzeru ndi chidziwitso, inkapeza kuti iwo anali oposa amatsenga ndi owombeza onse a mu ufumu wake wonse mopitirira muyeso.


achinyamata wopanda chilema, okongola, aluso mu nzeru zonse, okhala ndi chidziwitso, achangu pophunzira, odziwa kutumikira mʼnyumba ya mfumu. Ndipo anati awaphunzitsenso kuwerenga chiyankhulo cha Ababuloni.


Chaka chachitatu cha Koresi mfumu ya Aperezi, Danieli amene ankatchedwa Belitesezara analandira mawu a vumbulutso. Uthenga wake unali woona ndipo anawumvetsa movutikira. Uthengawu anawumva kudzera mʼmasomphenya.


Usiku Yehova anamuwululira Danieli chinsinsi chija mʼmasomphenya. Pamenepo Danieli anatamanda Mulungu wakumwamba,


Amasintha nthawi ndi nyengo; amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso. Amapatsa nzeru kwa anzeru ndi chidziwitso kwa ozindikira zinthu.


Ndikuyamika ndi kutamanda Inu Mulungu wa makolo anga: mwandipatsa nzeru ndi mphamvu, mwandiwululira zomwe tinakupemphani, mwatiwululira maloto a mfumu.”


Koma chinsinsi ichi chavumbulutsidwa kwa ine, si chifukwa chakuti ndili ndi nzeru zochuluka kuposa anthu ena onse, koma kuti mfumu mudziwe tanthauzo la maloto anu ndi kuti muzindikire maganizo amene anali mu mtima mwanu.


Choncho ndinalamula kuti anthu onse a nzeru a ku Babuloni abwere pa maso panga kunditanthauzira malotowo.


Ndamva kuti mzimu wa milungu uli mwa iwe ndi kuti uli ndi chidziwitso, luntha ndi nzeru zapadera.


Chaka choyamba cha ufumu wa Belisazara wa ku Babuloni, Danieli akugona pa bedi lake analota maloto ndipo anaona masomphenya. Iye analemba malotowo mwachidule.


Chaka chachitatu cha ulamuliro wa mfumu Belisazara, Ine Danieli, ndinaonanso masomphenya, ena atatha amene anandionekera poyamba.


Mulungu anati, “Mverani mawu anga: “Pakakhala mneneri wa Yehova pakati panu, ndimadzionetsera kwa iyeyo mʼmasomphenya, ndimayankhula naye mʼmaloto.


Pakuti Ine ndidzakupatsani mawu ndi nzeru kotero kuti palibe mmodzi wa adani anu adzathe kuwakana kapena kuwatsutsa.


Koma iwo sanathe kumugonjetsa chifukwa iye ankayankhula ndi nzeru zimene Mzimu Woyera anamupatsa.


ndipo anamupulumutsa iye kumasautso ake onse. Mulungu anamupatsa Yosefe nzeru ndi chisomo pamaso pa Farao mfumu ya ku Igupto, kotero mfumuyo inamuyika iye kukhala nduna yayikulu ya dziko la Igupto ndiponso nyumba yake yonse yaufumu.


Mose anaphunzira nzeru zonse za Aigupto, ndipo anali wamphamvu mʼmawu ndi ntchito zake.


Chifukwa cha ichi, kuyambira tsiku limene tinamva za inu, sitinasiye kukupemphererani ndi kumupempha Mulungu kuti akudzazeni ndi chidziwitso cha chifuniro chake kudzera mu nzeru yonse yauzimu ndi kumvetsetsa.


Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda.


Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa