Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 1:12 - Buku Lopatulika

12 nzeru ndi chidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso chuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhale nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 nzeru ndi chidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso chuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhale nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 nzeruzo ndi luntha ndikupatsa. Ndidzakupatsanso chuma, katundu ndi ulemu, zinthu zoti panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali nazo mwa mafumu amene analipo iwe usanabadwe, ndipo sipadzaonekanso wokhala nazo iweyo utafa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ine ndidzakupatsa nzeru ndi chidziwitso. Ndipo ndidzakupatsanso katundu, chuma ndi ulemu, zinthu zoti palibe mfumu imene inali nazo iwe usanakhalepo ndipo palibe wina amene adzakhale nazo iweyo ukadzafa.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 1:12
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu onse a padziko anafuna nkhope ya Solomoni, kudzamva nzeru zake zimene Mulungu analonga m'mtima mwake.


Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.


Ndipo Yehova anakuza Solomoni kwakukulu pamaso pa Aisraele onse, nampatsa ulemerero wachifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Israele inali nao wotero.


Momwemo mfumu Solomoni inaposa mafumu onse a padziko lapansi, kunena za chuma ndi nzeru.


Nanga Solomoni mfumu ya Israele sanachimwe nazo zinthu izi? Chinkana mwa amitundu ambiri panalibe mfumu ngati iye, ndi Mulungu wake anamkonda, ndi Mulungu wake anamlonga mfumu ya Aisraele onse; koma ngakhale iye, akazi achilendo anamchimwitsa.


Ndinakula chikulire kupambana onse anali mu Yerusalemu ndisanabadwe ine; ndipo nzeru yanganso inakhala nanebe.


Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lake ndi kukondwera ndi ntchito zake; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu.


Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.


Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,


Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa