Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 1:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo m'mau ali onse anzeru ndi aluntha, amene mfumu inawafunsira. Inawapeza akuposa alembi ndi openda onse mu ufumu wake wonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo m'mau ali onse anzeru ndi aluntha, amene mfumu inawafunsira. Inawapeza akuposa alembi ndi openda onse m'ufumu wake wonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Nthawi zonse mfumu ikawafunsa zonse zofuna nzeru ndi chidziwitso, inkapeza kuti iwo anali oposa amatsenga ndi owombeza onse a mu ufumu wake wonse mopitirira muyeso.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 1:20
25 Mawu Ofanana  

Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipiro anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andichitire ine choipa.


Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a mu Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.


Ndipo kunali, atafika Ayuda okhala pafupi pao ochokera pamalo ponse, anatiuza ife kakhumi, Bwererani kwa ife.


Kakhumi aka mwandichititsa manyazi; mulibe manyazi kuti mundiumira mtima.


Ndili nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse; pakuti ndilingalira mboni zanu.


Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.


Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.


Ndipo alembi anachita momwemo ndi matsenga ao, nakweretsa achule padziko la Ejipito.


Ndipo mzimu wa Ejipito adzakhala wachabe pakati pake; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wake; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta.


taona, ndiwe wanzeru woposa Daniele, palibe chinsinsi angakubisire;


Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.


M'mwemo chilamulirocho chidamveka, ndi eni nzeru adati aphedwe; anafunafunanso Daniele ndi anzake aphedwe.


pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira.


Pamenepo anayankha Daniele, nati kwa mfumu, Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphotho zanu mupatse wina; koma ndidzawerengera mfumu lembalo, ndi kumdziwitsa kumasulira kwake.


popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa