Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 2:19 - Buku Lopatulika

19 Pamenepo chinsinsicho chinavumbulutsidwa kwa Daniele m'masomphenya a usiku. Ndipo Daniele analemekeza Mulungu wa Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Pamenepo chinsinsicho chinavumbulutsidwa kwa Daniele m'masomphenya a usiku. Ndipo Daniele analemekeza Mulungu wa Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Usiku Yehova anamuwululira Danieli chinsinsi chija mʼmasomphenya. Pamenepo Danieli anatamanda Mulungu wakumwamba,

Onani mutuwo Koperani




Danieli 2:19
16 Mawu Ofanana  

M'malingaliro a masomphenya a usiku, powagwira anthu tulo tatikulu


Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye; ndipo adzawadziwitsa pangano lake.


Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.


Iye avumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye.


Ndipo kuti anauza asiye chitsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukadzatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira.


Belitesazara iwe, mkulu wa alembi, popeza ndidziwa kuti mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera, ndi kuti palibe chinsinsi chikusautsa, undifotokozere masomphenya a loto langa ndalotali, ndi kumasulira kwake.


Daniele ananena, nati, Ndinaona m'masomphenya anga usiku, taonani, mphepo zinai za mumlengalenga zinabuka pa nyanja yaikulu.


Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano aakulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi.


Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.


Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.


Ndipo mauwo anakomera ana a Israele pamaso pao; ndi ana a Israele analemekeza Mulungu, osanenanso za kuwakwerera ndi kuwathira nkhondo, kuliononga dziko lokhalamo ana a Rubeni ndi ana a Gadi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa