Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 6:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo sanathe kuipambana nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo sanathe kuilaka nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Koma adalephera kumgonjetsa, chifukwa iye ankalankhula ndi nzeru zochokera kwa Mzimu Woyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Koma iwo sanathe kumugonjetsa chifukwa iye ankayankhula ndi nzeru zimene Mzimu Woyera anamupatsa.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 6:10
18 Mawu Ofanana  

Pakuti ndadzazidwa ndi mau, ndi mzimu wa m'kati mwanga undifulumiza.


Koma m'munthu muli mzimu, ndi mpweya wa Wamphamvuyonse wawazindikiritsa.


Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi kukuphunzitsa chomwe ukalankhule.


Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.


Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipo adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova.


Koma pamene ndilankhula nawe ndidzatsegula pakamwa pako, nudzanena nao, Atero Yehova Mulungu. Wakumvera amvere, wosafuna kumvera akhale; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.


Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake.


Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.


Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.


Anyamatawo anayankha, Nthawi yonse palibe munthu analankhula chotero.


koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.


Pamenepo anafuna anthu akumpitira pansi, ndi kuti, Tidamumva iye alikunenera Mose ndi Mulungu mau amwano.


Koma anauka ena a iwo ochokera m'sunagoge wa Alibertino, ndi Akirene, ndi Aaleksandriya, ndi mwa iwo a ku Silisiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano.


Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu.


Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhale ndi mau okopa a nzeru, koma m'chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa