Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 7:1 - Buku Lopatulika

1 Chaka choyamba cha Belisazara mfumu ya ku Babiloni Daniele anaona loto, naona masomphenya a m'mtima mwake pakama pake; ndipo analemba lotolo, nalifotokozera, mwachidule.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Chaka choyamba cha Belisazara mfumu ya ku Babiloni Daniele anaona loto, naona masomphenya a m'mtima mwake pakama pake; ndipo analemba lotolo, nalifotokozera, mwachidule.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Chaka choyamba cha ufumu wa Belisazara wa ku Babuloni, Danieli akugona pa bedi lake analota maloto ndipo anaona masomphenya. Iye analemba malotowo mwachidule.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 7:1
34 Mawu Ofanana  

Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.


Ndipo Mulungu ananena kwa Israele, m'masomphenya a usiku, nati, Yakobo, Yakobo.


M'malingaliro a masomphenya a usiku, powagwira anthu tulo tatikulu


Tsopano pita, ukalembe mauwa pamaso pao pathabwa, nuwalembe m'buku, kuti akakhalebe kunthawi yam'tsogolo, mboni ya masiku onse.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Tenga iwe polembapo papakulu, nulembe pamenepo ndi malembedwe odziwika, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza.


Mneneri wokhala ndi loto, anene loto lake; ndi iye amene ali ndi mau anga, anene mau anga mokhulupirika. Kodi phesi ndi chiyani polinganiza ndi tirigu? Ati Yehova.


Ndipo amitundu onse adzamtumikira iye, ndi mwana wake, ndi mdzukulu wake, mpaka yafika nthawi ya dziko lake; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu aakulu adzamuyesa iye mtumiki wao.


Ndipo Yeremiya anatenga mpukutu wina, naupereka kwa Baruki mlembi, mwana wa Neriya; amene analemba m'menemo ponena Yeremiya mau onse a m'buku lija Yehoyakimu mfumu ya Yuda analitentha m'moto; ndipo anaonjezapo mau ambiri oterewa.


Ndipo Yeremiya anaitana Baruki mwana wa Neriya; ndipo Yeremiya analembetsa Baruki m'buku lampukutu mau onse a Yehova, amene ananena naye.


Ndipo kunali chaka cha makumi atatu, mwezi wachinai, tsiku lachisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.


M'masomphenya a Mulungu Iye anabwera nane m'dziko la Israele, nandikhalitsa paphiri lalitali ndithu; pamenepo panali ngati mamangidwe a mzinda kumwera.


Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.


Chaka chachiwiri cha Nebukadinezara mfumu, Nebukadinezarayo analota maloto, ndi mzimu wake unavutika, ndi tulo take tidamwazikira.


Mfumu inayankha, niti kwa Daniele, amene dzina lake ndiye Belitesazara, Ukhoza kodi kundidziwitsa lotolo ndidalilota, ndi kumasulira kwake?


Ndinaona m'masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba.


Ndinaona loto lakundiopsa, ndi zolingirira za pakama panga, ndi masomphenya a m'mtima mwanga, zinandivuta ine.


Mfumu Belisazara anakonzera anthu ake aakulu chikwi chimodzi madyerero aakulu, namwa vinyo pamaso pa chikwicho.


Ndipo inu mwana wake, Belisazara inu, simunadzichepetse m'mtima mwanu, chinkana munazidziwa izi zonse;


Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Ababiloni anaphedwa.


Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake.


Koma ine Daniele, mzimu wanga unalaswa m'kati mwa thupi langa, ndi masomphenya a m'mtima mwanga anandivuta.


Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano aakulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi.


Chaka chachitatu cha Belisazara mfumu masomphenya anandionekera kwa ine Daniele, atatha kundionekera oyamba aja.


Ndipo kudzachitika m'tsogolo mwake, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya;


Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.


Ndipo Yehova anandiyankha nati, Lembera masomphenyawo, nuwachenutse pamagome, kuti awawerenge mofulumira.


Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.


Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.


Ndiyenera kudzitamandira, kungakhale sikupindulika; koma ndidzadza kumasomphenya ndi mavumbulutso a Ambuye.


Chifukwa chake lemba zimene unaziona, ndi zimene zilipo, ndi zimene zidzaoneka m'tsogolomo;


Ndipo pamene adalankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndinati ndilembe; ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba nanena, Sindikiza nacho chizindikiro zimene adalankhula mabingu asanu ndi awiri, ndipo usazilembe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa