Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 1:10 - Buku Lopatulika

10 Mundipatse tsono nzeru ndi chidziwitso, kuti ndituluke ndi kulowa pamaso pa anthu awa; pakuti angathe ndani kuweruza anthu anu awa ambiri?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Mundipatse tsono nzeru ndi chidziwitso, kuti ndituluke ndi kulowa pamaso pa anthu awa; pakuti angathe ndani kuweruza anthu anu awa ambiri?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsono mundipatse nzeru ndi luntha, kuti ndiŵatsogolere bwino anthu anuŵa. Nanga popanda nzeruzo ndani angathe kulamulira mtundu waukulu wa anthu anu?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Mundipatse nzeru ndi luntha zolamulira anthu awa, pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 1:10
14 Mawu Ofanana  

Masiku anapitawo, pamene Saulo anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisraele kutuluka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israele, ndi kukhala mtsogoleri wa Israele.


Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?


Chokhachi, Yehova akupatse nzeru ndi luntha, nakulangize za Israele, kuti usunge chilamulo cha Yehova Mulungu wako.


Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.


Manja anu anandilenga nandiumba; mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu.


Nzeru ipambana, tatenga nzeru; m'kutenga kwako konseko utenge luntha.


Mwa ine mafumu alamulira; akazembe naweruza molungama.


wakutuluka pamaso pao, ndi kulowa pamaso pao, wakuwatulutsa ndi kuwalowetsa; kuti khamu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.


koma kwa ena fungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi?


si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu;


nati nao, Ndine munthu wa zaka zana ndi makumi awiri lero lino; sindikhozanso kutuluka ndi kulowa; ndipo Yehova anati kwa ine, Sudzaoloka Yordani uyu.


Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa