Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.
2 Samueli 6:20 - Buku Lopatulika Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yake. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anatulukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israele inalemekezeka ndithu, amene anavula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ake, monga munthu woluluka avula wopanda manyazi! Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yake. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anatulukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israele inalemekezeka ndithu, amene anavula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ake, monga munthu woluluka avula wopanda manyazi! Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Davide adabwerera kuti akadalitse banja lake, Mikala, mwana wa Saulo, adadzamchingamira nati, “Nkutero mfumu ya Aisraele kudzilemekeza kwake lero! Mpaka kuchita kudzivula pamaso pa adzakazi a antchito ake, monga m'mene amachitira munthu wamisala, opanda ndi manyazi omwe!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide atabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake, Mikala mwana wamkazi wa Sauli anatuluka kudzakumana naye ndipo anati, “Kodi mfumu ya Israeli ingatero kudzilemekeza kwake lero, kudzithyolathyola pamaso pa akapolo aakazi, antchito ake ngati munthu wamba.” |
Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.
Ndipo Davide anavina ndi mphamvu yake yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta.
Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake.
Pamene Davide adatsiriza kupereka nsembe yopsereza ndi zoyamika, iye anawadalitsa anthuwo m'dzina la Yehova wa makamu.
Ndipo anagawira anthu onse, ndiwo unyinji wonse wa Israele, amuna ndi akazi, kwa munthu yense mtanda wa mkate ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa. Ndipo anthu aja onse anabwera yense kunyumba yake.
Ndidzachita mwanzeru m'njira yangwiro; mudzandidzera liti? Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.
Ndipo pamene Petro anali pansi m'bwalo, anadzapo mmodzi wa adzakazi a mkulu wa ansembe;
Anadza pomwepo kwa Simoni Petro. Iyeyu ananena ndi Iye, Ambuye, kodi Inu mundisambitsa ine mapazi?
Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.
Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m'nyumba ya Baala-Beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pake ndi opepuka amene anamtsata.
Ndipo ana a Saulo ndiwo Yonatani, ndi Isivi, ndi Malikisuwa; ndi maina a ana aakazi ake awiri ndi awa: dzina la woyamba ndiye Merabi, ndi dzina la mng'ono wake ndiye Mikala;
Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anakonda Davide; ndipo pakumva Saulo, anakondwera nako.