2 Samueli 6:19 - Buku Lopatulika19 Ndipo anagawira anthu onse, ndiwo unyinji wonse wa Israele, amuna ndi akazi, kwa munthu yense mtanda wa mkate ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa. Ndipo anthu aja onse anabwera yense kunyumba yake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Ndipo anagawira anthu onse, ndiwo unyinji wonse wa Israele, amuna ndi akazi, kwa munthu yense mtanda wa mkate ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa. Ndipo anthu aja onse anabwera yense kunyumba yake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Kenaka adagaŵira Aisraele onsewo, amuna ndi akazi, aliyense mtanda wa buledi, nthuli yanyama, ndiponso keke ya mphesa zouma. Tsono anthu onse adachokapo, napita aliyense kunyumba kwake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Kenaka iye anagawira Aisraeli onsewo, aamuna ndi aakazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama, ndiponso keke yamphesa zowuma. Ndipo anthu onse anachokapo, napita aliyense ku nyumba kwake. Onani mutuwo |
Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.