Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 6:20 - Buku Lopatulika

20 Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yake. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anatulukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israele inalemekezeka ndithu, amene anavula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ake, monga munthu woluluka avula wopanda manyazi!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yake. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anatulukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israele inalemekezeka ndithu, amene anavula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ake, monga munthu woluluka avula wopanda manyazi!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Pamene Davide adabwerera kuti akadalitse banja lake, Mikala, mwana wa Saulo, adadzamchingamira nati, “Nkutero mfumu ya Aisraele kudzilemekeza kwake lero! Mpaka kuchita kudzivula pamaso pa adzakazi a antchito ake, monga m'mene amachitira munthu wamisala, opanda ndi manyazi omwe!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Davide atabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake, Mikala mwana wamkazi wa Sauli anatuluka kudzakumana naye ndipo anati, “Kodi mfumu ya Israeli ingatero kudzilemekeza kwake lero, kudzithyolathyola pamaso pa akapolo aakazi, antchito ake ngati munthu wamba.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 6:20
23 Mawu Ofanana  

Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.


Ndipo Davide anavina ndi mphamvu yake yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta.


Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake.


Pamene Davide adatsiriza kupereka nsembe yopsereza ndi zoyamika, iye anawadalitsa anthuwo m'dzina la Yehova wa makamu.


Ndipo anagawira anthu onse, ndiwo unyinji wonse wa Israele, amuna ndi akazi, kwa munthu yense mtanda wa mkate ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa. Ndipo anthu aja onse anabwera yense kunyumba yake.


Ndipo anachoka anthu onse, yense kunyumba yake, nabwera Davide kudalitsa nyumba yake.


Ndiwo ana a opusa, inde ana a anthu opanda dzina; anawaingitsa kuwachotsa m'dziko.


Ndidzachita mwanzeru m'njira yangwiro; mudzandidzera liti? Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.


Ndidzakukwezani, Yehova; pakuti mwandinyamutsa, ndipo simunandikondwetsere adani anga.


Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa; uferenji nthawi yako isanafike?


Ndipo pamene Petro anali pansi m'bwalo, anadzapo mmodzi wa adzakazi a mkulu wa ansembe;


Ndipo pamene abale ake anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaluka.


Anadza pomwepo kwa Simoni Petro. Iyeyu ananena ndi Iye, Ambuye, kodi Inu mundisambitsa ine mapazi?


Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.


Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m'nyumba ya Baala-Beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pake ndi opepuka amene anamtsata.


Ndipo ana a Saulo ndiwo Yonatani, ndi Isivi, ndi Malikisuwa; ndi maina a ana aakazi ake awiri ndi awa: dzina la woyamba ndiye Merabi, ndi dzina la mng'ono wake ndiye Mikala;


Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anakonda Davide; ndipo pakumva Saulo, anakondwera nako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa