Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 3:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo pamene abale ake anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaluka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo pamene abale ake anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaluka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Achibale ake atamva zimenezi, adabwera kuti adzamtenge, chifukwa ankati, “Wachita misala.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Anthu a ku banja lake atamva zimenezi, anapita kuti akamutenga, pakuti ankanena kuti, “Wazungulira mutu.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 3:21
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehu anatulukira kwa anyamata a mbuye wake, nanena naye wina, Mtendere kodi? Anakudzera chifukwa ninji wamisala uyu? Nanena nao, Mumdziwa munthuyo ndi makambidwe ake.


Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'goli.


Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israele adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, chifukwa cha kuchuluka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukulu.


Ndipo anadza amake ndi abale ake; naima kunja, namtumira uthenga kumuitana.


Koma ambiri mwa iwo ananena, Ali ndi chiwanda, nachita misala; mukumva Iye bwanji?


Koma pakudzikanira momwemo, Fesito anati ndi mau aakulu, Uli wamisala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakuchititsa misala.


Pakuti ngati tili oyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tili a nzeru zathu, titero kwa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa