Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 3:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Belezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Belezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Aphunzitsi ena a Malamulo, amene adaabwera kuchokera ku Yerusalemu, ankanena kuti, “Munthu ameneyu wagwidwa ndi Belezebulu.” Ankatinso, “Mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa nzochokera kwa mkulu wa mizimuyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Ndipo aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anati, “Iye wagwidwa ndi Belezebabu! Ndi ulamuliro wa mkulu wa ziwanda akutulutsa ziwanda.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 3:22
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pamwamba pa chipinda chake chosanja chinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni ngati ndidzachira nthenda iyi.


Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai, chotonza cha anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.


Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamutcha mwini banja Belezebulu, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake?


Pakuti Yohane anadza wosadya, wosamwa, ndipo iwo amati, Ali ndi chiwanda.


Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebulu, mkulu wa ziwanda.


Pomwepo anadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, ochokera ku Yerusalemu, nati,


Koma Afarisi analinkunena, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda.


Ndipo anasonkhana kwa Iye Afarisi, ndi alembi ena, akuchokera ku Yerusalemu,


Koma ena mwa iwo anati, Ndi Belezebulu mkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda.


Ndipo panali tsiku limodzi la masiku awo, Iye analikuphunzitsa; ndipo analikukhalapo Afarisi ndi aphunzitsi a malamulo, amene anachokera kumidzi yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndi Yerusalemu: ndipo mphamvu ya Ambuye inali ndi Iye yakuwachiritsa.


Koma kunali phwando la kukonzetsanso mu Yerusalemu; nyengoyo ndi yachisanu.


Khamu la anthu linayankha, Muli ndi chiwanda: afuna ndani kukuphani Inu?


Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda?


Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa kunthawi yonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa