Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 7:17 - Buku Lopatulika

17 Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa; uferenji nthawi yako isanafike?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa; uferenji nthawi yako isanafike?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Usachite kunyanyanso kuipa, usanyanye nawonso uchitsiru. Nanga uferenji nthaŵi yako isanakwane?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Usakhale woyipa kwambiri, ndipo usakhale chitsiru, uferenji nthawi yako isanakwane?

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 7:17
15 Mawu Ofanana  

Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yake. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anatulukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israele inalemekezeka ndithu, amene anavula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ake, monga munthu woluluka avula wopanda manyazi!


Amene anakwatulidwa isanafike nyengo yao, chigumula chinakokolola kuzika kwao;


Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.


Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku; koma zaka za oipa zidzafinimpha.


Unatenganso ana ako aamuna ndi aakazi amene unandibalirawo, ndi kuwapereka nsembe awathe. Zigololo zako zidachepa kodi,


Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Chinthu chopepuka ichi kodi ndi nyumba ya Yuda, kuti achite zonyansa azichita kunozi? Pakuti anadzaza dziko ndi chiwawa, nabwereranso kuutsa mkwiyo wanga, ndipo taonani, aika nthambi kumphuno kwao.


Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, chifukwa sanampatse Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.


Koma Paulo anafuula ndi mau aakulu, nati, Usadzipweteka wekha; tonse tili muno.


Ndipo anagwa pansi pomwepo pa mapazi ake, namwalira; ndipo analowa anyamatawo, nampeza iye wafa, ndipo anamnyamula kutuluka naye, namuika kwa mwamuna wake.


Koma Ananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha aakulu anagwera onse akumvawo.


Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.


Ndipo kunali, atapita masiku khumi, Yehova anamkantha Nabala, nafa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa